Ndipo munthu anaponya mubvi wace ciponyeponye, namlasa pakati pa maluma a maraya ace acitsulo. Potero anati kwa woyendetsa garetayo, Tembenuza dzanja lako, nundicotse ku khamu la nkhondo kuno, pakuti ndalasidwa.