Nati iye, Ndinaona Aisrayeli onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; nati Yehova, Awa alibe mbuye wao, abwerere yense ku nyumba yace mumtendere.