Pakuti Alevi anasiya podyetsa pao, ndi maiko ao ao, nadza ku Yuda ndi ku Yerusalemu; popeza Yerobiamu ndi ana ace anawataya, kuti asacitire Yehova nchito ya nsembe;