Ndipo kunacitika, monga adanena munthu wa Mulungu kwa mfumu, ndi kuti, Adzagula miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, adzagulanso muyeso wa ufa ndi sekeli; kudzatero mawa, dzuwa lino, pa cipata ca Samariya;