Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Moabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Moabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako.