Ndipo pamene anampenya ana a aneneri okhala ku Yeriko pandunji pace, anati, Mzimu wa Eliya watera pa Elisa. Ndipo anadza kukomana naye, nadziweramitsa pansi kumaso kwace.