Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yoa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu m'Ciaramu; popeza ticimva ici; musalankhule nafe m'Ciyuda, comveka ndi anthu okhala palinga.