Macitidwe ena tsono a Yerobiamu, ndi zonse anazicita, ndi mphamvu yace, umo anacita nkhondo, nabweza kwa Israyeli Damasiko ndi Hamati amene anali a Yuda, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?