Macitidwe ena tsono a Yoasi adazicita, ndi mphamvu yace, ndi umo analimbana naye Amaziya mfumu ya Yuda, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?