Ndi Yoasi mwana wa Yoahazi analandanso m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaeli midzi ija adailanda m'dzanja la Yoahazi atate wace ndi nkhondo. Yoasi anamkantha katatu, naibweza midzi ya Israyeli.