Koma Yehova analeza nao mtima, nawacitira cifundo, nawatembenukira; cifukwa ca cipangano cace ndi Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pace.