Ndipo atsogoleri a mazana anacita monga mwa zonse anawalamulira Yehoyada wansembe, natenga yense anthu ace olowera pa Sabata, ndi oturukira pa Sabata, nafika kwa Yehoyada wansembeyo.