Pamenepo mfumu inatuma kwa iye asilikari makumi asanu ndi mtsogoleri wao. Iye nakwera kumka kwa Eliya; ndipo taonani, analikukhala pamwamba pa phiri. Ndipo analankhula naye, Munthu wa Mulungu iwe, mfumu ikuti, Tsika.