Ndipo Ahaziya anagwa kubzola ku made wa cipinda cace cosanja cinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni ngati ndidzacira nthenda iyi.