Ndipo anauka mamawa; ndipo kutaca, Samueli anaitana Sauli ali pamwamba pa nyumba, nati, Ukani kuti ndikuloleni mumuke. Ndipo Sauli anauka, naturuka onse awiri, iye ndi Samueli, kunka kunja.