Ndipo Sauli anayankha nati, Sindiri Mbenjamini kodi, wa pfuko laling'ono mwa Israyeli? Ndiponso banja lathu nlocepa pakati pa mabanja onse a pfuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine?