Ndipo anthu a ku Kiriati-yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wace wamwamuna Eleazeri kuti asunge likasa la Yehova.