Ndipo iye anamucha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wacoka kwa Israyeli; cifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi cifukwa ca mpongozi wace ndi mwamuna wace.