Ndipo Afilisti anaponyana nao, nakantha Aisrayeli; iwowa nathawira, munthu yense ku hema wace; ndipo kunali kuwapha kwakukuru; popeza anafako Aisrayeli zikwi makumi atatu a oyenda pansi.