Pamenepo Davide ananena naye, Ndiwe wa yani? ufumira kuti? Nati iye, Ndiri mnyamata wa ku Aigupto, kapolo wa M-amaleki; mbuye wanga anandisiya, cifukwa ndinayambodwala apita masiku atatu.