Ndipo Davide ndi anthu ace anakwera, nathira nkhondo yobvumbulukira pa Agesuri, ndi Agirezi, ndi Aamaleki; pakuti awa ndiwo anthu akale a m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Aigupto.