Ndipo iwo ananyamuka, namuka ku Zifi asanapiteko Sauli; koma Davide ndi anthu ace anali ku cipululu ca Maoni, m'cigwa ca kumwera kwa cipululu.