Mfumu niuza asilikari akuima comzinga iye, Potolokani, iphani ansembe a Yehova; cifukwa agwirizana ndi Davide, ndipo anadziwa kuti alinkuthawa, koma sanandiululira. Koma anayamata a mfumu sanafuna kutambalitsa manja ao kupha ansembe a Yehova.