Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ace anacitira Aisrayeli onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo la cihema cokomanako.