Ndipo Sauli anatumiza mithenga ku nyumba ya Davide imdikire, ndi kumupha m'mawa; koma Mikala mkazi wa Davide anamuuza, nati, Ukapanda kupulumutsa moyo wako usiku uno, udzaphedwa ndithu m'mawa.