Ndipo anyamata a Sauli analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muciyesera cinthu copepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndiri munthu wosauka, ndi wopeputsidwa.