Ndipo kunali kuti pamene mzimu woipawo wocokera kwa Mulungu unali pa Sauli, Davide anatenga zeze, naliza ndi dzanja lace; comweco Sauli anatsitsimuka, nakhala bwino, ndi mzimu woipa unamcokeraiye.