Tsono inu mbuye wathu muuze anyamata anu, amene ali pamaso panu, kuti afune munthu wanthetemya wodziwa kuyimba zeze; ndipo kudzakhala, pamene mzimu woipa wocokera kwa Mulungu uli pa inu, iyeyo adzayimba ndi dzanja lace, ndipo mudzakhala wolama.