Pomwepo iye anati, Ndinacimwa, koma mundicitire ulemu tsopano pamaso pa akuru a anthu anga, ndi pamaso pa Israyeli, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu.