Ndikalipo ine; citani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wace; ndinalanda ng'ombe ya yani? kapena ndinalanda buru wa yani? ndinanyenga yani? ndinasautsa yani? ndinalandira m'manja mwa yani cokometsera mlandu kutseka naco maso anga? ngati ndinatero ndidzacibwezera kwa inu.