1. Ndipo Davide anati, Pano padzakhala nyumba ya Yehova Mulungu, ndi pano padzakhala guwa la nsembe yopsereza la Israyeli.
2. Ndipo Davide anati asonkhanitse alendo okhala m'dziko la Israyeli; iye naika osema miyala afukule miyala, aiseme kuti amange nayo nyumba ya Mulungu.
3. Nakonzeratu Davide citsulo cocuruka ca misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wocuruka wosauyesa kulemera kwace;
4. ndi mitengo yamikungudza yosaiwerenga; pakuti Asidoni ndi Aturo anabwera nayo kwa Davide mitengo yamikungudza yocuruka,