Ndipo m'kati mwa monenera m'menemo, m'litali mwace munali mikono makumi awiri, kupingasa kwace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mikono makumi awiri; ndipo anamukuta ndi golidi woyengetsa, nakutanso guwa la nsembe ndi matabwa amkungudza,