Ndipo anawatuma ku Lebano mwezi umodzi zikwi khumi kuwasintha, mwezi umodzi iwo anali ku Lebano, miyezi iwiri anali kwao; ndipo Adoniramu anali kapitao wa athangata.