26. Pamenepo inati mfumu ya Israyeli, Tengani Mikaya, mumbweze kwa Amoni kalonga wa mudzi, ndi kwa Yoasi mwana wa mfumu;
27. ndipo muziti, Itero mfumu, Khazikani uyu m'kaidi, mumdyetse cakudya ca nsautso, ndi madzi a nsautso, mpaka ndikabwera ndi mtendere.
28. Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhula mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.
29. Tsono mfumu ya Israyeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera ku Ramoti Gileadi.
30. Ndipo mfumu ya Israyeli inanena ndi Yehosafati, Ine ndidzadzizimbaitsa, ndi kulawa kunkhondo, koma bvala iwe zobvala zako zacifumu. Ndipo mfumu ya Israyeli inadzizimbaitsa, nilowa kunkhondo.