Tsono mthenga uja udakaitana Mikaya unanena naye, nati, Taona, mau a aneneri abvomerezana zokoma kwa mfumu ndi m'kamwa m'modzi; mau ako tsono afanane ndi mau a wina wa iwowo, nunene zabwino.