Ndipo anthu aja a mudzi wace, ndiwo akulu ndi omveka adakhala m'mudzi mwace, anacita monga Yezebeli anawatumizira, monga munalembedwa m'akalata amene iye anawatumizira.