Ndipo Ahabu anakadya, namwa; koma Eliya anakwera pamwamba pa Karimeli, nagwadira pansi, naika nkhope yace pakati pa maondo ace.