Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitoreti mulungu wa Azidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amoabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kucita cimene ciyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wace.