Mpandowo wacifumu unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndi pamwamba pa mpando wacifumu panali pozungulira kumbuyoko, ndipo munali ngati manja m'mbali zonse ziwiri za pokhalirapo, naimika mikango iwiri m'mbali mwa manjawo.